CHIMANGA

Zoyenera Kudziwa Paulimi Wachimanga

Chimanga chimakula bwino mu nthaka yosasunga madzi, nthaka ya chonde, komanso kumadela komwe mvula imagwa kudutsa 500mm.

Pewani:

Kukonza munda

Konzani munda mvula ikangotha kapena pamene mwamaliza kukolola. Tipulani mozamitsa bwino kuti zotsalira mmunda ziwolerane bwino komanso kuti mpweya udzitha kudutsa bwino.

Mizere

Pokonza mizere, onetsetsani kuti mizere yatalikirana 75cm kuchoka pamzere kufika pa mzere wina. Ndipo mizereyo ikhale yokwera 30cm kuchoka pansi. Pamalo otsetsereka, konzani mizere mopingasa.

[chimanga_image1]

Kuthila Manyowa

Alimi akulimbikitsidwa kugwirisa ntchito manyowa. Manyowa amaonjezera chonde mu nthaka komanso kufewetsa nthaka.

Thirani manyowa mwezi umodzi kapena kupitilira apo musanabzale. Thirani manyowa okwanira matani asanu (5) pa ekala imodzi; kapena matani khumi ndi awiri ndi theka (12.5)pa hekitala imodzi. Thirani manyowa odzadza ndowa mukhwawa lotalika ma mitala asanu ndi atatu (8m).

Ngati muli ndimanyowa ochepa, thirani kawiri manyowa odzadza manja awiri pa phando ndipo sakanizani ndi dothi.

Mukhozanso kupanga manyowa a kompositi kuchokera kuzinyalala zowolerana zapanyumba komanso zakumunda.

Kuthila Fetereza

Kuti mupeze phindu la feteleza, choyambirira yezetsani nthaka yanu kuti mudziwe michere kapena mitundu ya feteleza yofunika m’munda mwanu. Funsani alangizi a m’dera lanu kuti akuthandizeni.

Thirani fetereza pamapando otalikirana ma sentimitala khumi (10cm) ndipo phando lirironse lizame masentimitala khumi (10cm).

Mtunda wothirira fetereza

Thirani fetereza wokulitsa pomwe mukudzala kapena pasanathe sabata imodzi mbeu ikangomera.

Thirani fetereza wachiwiri pakadutsa masabata atatu kapena anayi kuchokera pa tsiku lodzalira.

Kupalira

Palirani munda wanu mwachangu udzu ukangomera, chifukwa udzu umalimbirana ndi mbewu yanu chakudya chamthaka komanso madzi.

Tetezani chimanga ku udzu pogwiritsa ntchito njira yongozula kapena mankhwala, kapena kuphatikiza njira zonse. Palirani udzu kosachepera kawiri pamasabata asanu ndi imodzi (6) chimanga chikangomera.

Kugwiritsa ntchito makasu ndi manja

Palirani kapena zulirani udzu koyamba masabata awiri asanathe, ndipo kupalira kwachiwiri kuchitike masabata asanu ndi imodzi (6) asanathe kapena pamene mwaona kuti udzu wamera.

Phimbirani nthaka ndi mapesi kapena udzu omwe ulibe njere, chifukwa udzu wanjere umafesa njere zake zomwe zimachulukitsa vuto la udzu m’chaka chotsatira.

Palirani pamene kuli dzuwa ndipo pewani kupalira pamene mvula ikugwa chifukwa udzu siumafa.

Njira zina zochepetsera udzu ndi izi:

Kasinthasintha wa mbeu,

Onetsetsani kuti mmunda wanu mulibe udzu nthawi zonse.

 

Kugwiritsa ntchito mankhwala

Pali mitundu iwiri ya mankhwala yomwe imagwiritsidwa ntchito kupha udzu; Pali mankhwala opha njere komanso pali mankhwala opha udzu ukamera. Afunseni alangizi za mankhwala oyenera kuthira ndi kathiridwe kake. Mankhwala opha njere kapena udzu athiridwe dothi likadali ndichinyontho.

Welengani bwino ndikutsatira malangizo akagwiritsidwe ntchito kamankhwalawa amene alembedwa pabotolo.

Gulani mankhwala ku malo ovomerezeka!!!!

|Back |Home | Up|